Mr Hez

Mr Hez Contact information, map and directions, contact form, opening hours, services, ratings, photos, videos and announcements from Mr Hez, Carpenter, Machinjiri, Blantyre.

20/09/2025
Ndimusungile skeva azaone akazakula
10/08/2025

Ndimusungile skeva azaone akazakula

12/06/2025

*Dzulo ndatumiza K30,000 kunambala yolakwika mwangozi ine shaaa🤔🤔 ndipange bwanj kuti ndalama ya ibwelere🙆🏿‍♂️ Ndinaganiza plan ndipo ndinalemba SMS yoti;*
"Tathokoza ngati mulibwino🤝 Tatumiza ndalama izo kuchokela Ku bungwe la satanic, madzulo ano mukalumbilitsidwa komaso kwa m'bale wanu modzi asowa ndipo kuchitika maliro azizizi. Imeneyo ngati nsembe yanu. Ngati simuli okozeka kuti-joina satanic chonde bwezani ndalamazo pasanathe 15 minutes.

*Chandiyakha kuti; 🗣️ brother mutumizeso K60,000 kwapezeka azanga awiri nawoso akufuna kujoina.*

🙆🏿‍♂️hamayooooo ndalama zanga zqpita😭😫*

Follow 👉Mr Hez kuti tizicheza kumeneko kwinaku

06/06/2025



Anthu okwiya m'boma la Balaka apha bambo wazaka 29 pomuganizira kuti anaba ufa wachimanga, Soya Pieces, komanso Sipika.

M'neneri wa apolisi ya mbomalo Inspector Gladson M'bumpha, wati malemuyu ndi Rodrick Jackson yemwe wakhala akuvutitsa m'mudzi mwa Chibwana mfumu yaikulu Nsamala ndi mchitidwe wa umbanda ndipo wangotuluka kumene ku ndende ya Chichiri masabata apitawa.

M'bumpha wati Jackson anagwidwa pa 4 June chaka chino, kunyumba ya a Pilirani Luka komwe anaba katunduyi ndipo anthu okwiya anamumenya ndikumupha ndikukamutaya pafupi ndi nyumba ya nkazi wake.

Malipoti achipatala akusonyeza kuti malemuwa amwalira kaamba koti anataya magazi kwambiri m'mutu ndipo Apolisi ali mkati mosaka anthu oganiziridwawa kuti akukhuzidwa ndi imfayi.

Wolemba Bernike Gomani

  . Mtsogoleri wakale wa dziko la Zambia, Edgar Lungu wamwalira. Maripoti omwe tapeza akuonetsa kuti a Lungu amwalira ak...
05/06/2025


.

Mtsogoleri wakale wa dziko la Zambia, Edgar Lungu wamwalira.

Maripoti omwe tapeza akuonetsa kuti a Lungu amwalira akulandira thandizo la chipatala m'dziko la South Africa.

Lungu ndi mtsogoleri wanambala 6 wa dzikolo komanso wapampando wa mgwirizano wa zipani za ndale otchedwa Tonse.

Boma la Zambia silinalankhulepo pa imfayi.

Wolemba: Evance Rhonex Matola - Blantyre.

  Dziko la Tanzania lati laimitsa kaye tsamba la mchezo la Internet la X lomwe limadziwika kuti (Twitter) kwa kanthawi k...
05/06/2025



Dziko la Tanzania lati laimitsa kaye tsamba la mchezo la Internet la X lomwe limadziwika kuti (Twitter) kwa kanthawi kuti boma liunikirenso zinthu zina zomwe zimayikidwa pa tsambali.

Malinga ndi BBC, boma la Tanzania lapanga ganizo ili kamba kakuchuluka kwa zinthu zolawula pa X.

Wolemba: Laston Thefe'las Ingolo.

Apolisi M'boma la Mzimba akusaka Munthu amene wagwililila ndikupha Gogo Wezzi Nyasulu usiku wapitawuMa report ati munthu...
03/06/2025

Apolisi M'boma la Mzimba akusaka Munthu amene wagwililila ndikupha Gogo Wezzi Nyasulu usiku wapitawu

Ma report ati munthuyi analowa mnyumba mwa gogo Wezzi usiku wathawu ndi cholinga chofuna kukaba koma poti sanapeze chokuti Abe anachitila chipongwe gogoyi ndipo atamaliza zaupanduzi anawatsekela mnyumba momwemo kufikila kutacha pamene anthu anadabwa kuti gogowa sakudzuka
Atatchola chitseko anapeza kuti gogoyu wamwalila ndipo mapazi a munthu wachiwembuyo atadinda mnyumbamo

Poyankhula ndi mdzukulu wa Malemuwa wati pakadali Pano thupi la Malemuwa apita nalo Ku Mzuzu central hospital kuti akalipime zina ndi zina.

Hezrone carpentry and joinary+265999597353+265882208155Machinjiri Area 6 Maranatha
02/06/2025

Hezrone carpentry and joinary
+265999597353
+265882208155
Machinjiri Area 6 Maranatha

Address

Machinjiri
Blantyre

Website

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when Mr Hez posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Share

Category